Mnyamata afa atamuombera kunyumba za apolice

MNYAMATA AFA ATAMUOMBERA KUNYUMBA ZA POLICE

Mnyamata wa zaka 14, yemwe anali ophunzira mu Sitandade 8, wafa atamuwombera ndi mfuti mkati mwa nyumba za polisi ya Nkhunga, Dwangwa m’boma la NKhotakota.

Mneneri wa polisi ya Nkhunga Sub inspector Labani Makalani watsimikiza zakuombeledwa kwa Blessings Masimbo, yemwe masana Lachisanu .

A Makalani ati pakadali pano sangafotokoze zambiri kamba koti akufufuzabe za yemwe waombera mwanayu, cholinga chake komanso mtundu wa mfuti yomwe inagwiritsidwa ntchito.

Koma kalata yafotokoza kuti apolisi akuganiza kuti Blessings anawomberedwa ndi mwangozi ndi mnzake oyandikana naye nyumba yemwe amacheza naye.

Oganiziridwa mlanduyo ndi mwana wa wapolisi yemwe akuti amaseweretsa mfuti ya bamboo.

Blessings amachokera kwa Mfumu Kapoloma m’boma la Machinga.

 

 

Advertisements