Kubwalo LA masewera ampira kunaveka chimphokoso

 

Kubwalo lamasewera ampira kunamveka chiphokoso,

chakukondwerera ndi kusangalala, moti aliyense amene

sanapite anadziwiratu kut phokoso limeneli ndiye kuti

timu yathu ikupambana basi, ndiye kut timu yobwera

tikuigonjesa.

….

Mpira utatha anthube anali ndi nkhope za chimwemwe

kusonyeza kut zinthu zayenda bwino…, koma zinali

zodabwitsa atafunsidwa kut masewera atha bwanji,

onse amayankha kuti mpira wathera draw 0-0.

Ndiye kunali kufunsa kut phokoso limene lija and

mukuonekanso achimwemwe pamene masewero athera

draw?

Akut eya phokoso limene lija linali kut goalkeeper

wathu anagwira penalty.

Ndimene inalili timuyo tikuyenera kusangalala chifukwa

ndi timu yoti yagwetsa matimu ochuka akulu akulu

koma ife tuchiyesa chachimwemwe angakhale wathera

0-0

M’bale wanga pa Moyo wathu pali zambiri zomwe

zimachitika pali zoopsa zomwe zimaikika kut ziononge

moyo wathu panthawi yomwe tikugona kaya paulendo

kaya kuntchito kwathu ndi malo ochezera.., koma

pamakhala wina yemwe amalimbana nkugwira zonsezi

kut zisatichitikire.

Mukuziwa kut kaamba ka tsiku lalero tili ndi reason

yosangalala kumuyamika Ambuye angakhale moyo

wathu ukuonekabe kuti uli pa zero? Pali anthu ena

ochuka, andalama koma anagonjesewa ndi oipayo ena

tunena pano akusowa ntendere muzipatala zochuka

koma ife ngakhale tikuoneka tilibe kanthu, olira, akafa

nsiyanji koma tili naobe moyo wabwino wathanzi

kaamba koti Mbuye wathu watiteteza kuzambiri.

Tiyeni nthawi zonse angakhale zikuoneka kut

sizikuyenda tiyeni titenge gawo nkumuyamika kaamba

ka moyo okhawu omwe tili nao, Pali abale ambiri

anafunitsitsa atakhala ndi moyo koma sizinatheke ife

ndife okonderedwa sikuti tili ndi kuthekera kuli konse

kuti ndiife anzeru koma kuti Ambuye ali ndi cholinga

paife.

Amen

Advertisements