Mnyamata wins anapalana ubwezi ndi msungwana wina

 

Mnyamata wina anapalana ubwenzi ndi msungwana wina mdera lakwawo-poti mnyamatayo analibe ndalama masten a msungwanayo atanva anakwiya nazo heavy moti amati akakuma ndi mnyamatayo amamu lalatira koophya pa gulu komaso mwana wawoyo amamumenya kwambili kuti amusiye mamunayo koma sizimatheka-tsiku lina mnyamatayu atakumana ndi bwenzi lakeli anadabwa kunva zomwe msungwana wakeyu ananena”sory ndapeza wina iwe nanga mesa suli pa ntchito nanga ndiliti uzaipeze poti uli ndi MSCE yokha? Mnyamatayu anazizidwa nazo izi ndipo amaganiza ngati zocheza-

Patadusa masabata awili ananva komaso kuzionera yekha kuti msungwanayudi ali ndi mamuna wina owoneka osamba-apatu mnyamata auyamba mowa-midoli ndi win plus shooter kumwa size kukana-tsiku lina anamwa heavy nde nkukumana ndi msungwana uja akutsika galimoto la mamuna wake pamozi ndi mamuna wake uja apatu ndi mowa ndi mowa ana muuza mamuna winayo kut amusiye nkaziyo”apa mamuna osambayo ananena mmaso muli gwaa”iwe uli ndi chani kape iwe”apa mowa unathawa mmutu ndipo misozi inalengeza mmaso

Atafika kwawo mnyamatayo anangofikila pa mphasa yake apa maganizo oyipa anampeza ofuna imfa basi koma ataganiza bwino anaona kuti sibwinoso kutero apa anangoyambapo waku church- abusa anamupempherela kenako iyee analapa atalapa abusawo anamuuza kuti apemphere yekha amuuze mulungu zomwe iye akufuna apa mnyamata analila pamaso pa mulungu mu pemphero misozi yosamba inatuluka kwa 3 hours kenako anauyamba wakunyumba poti unali madzulo ka mdima katayamba

Ali munjila anaona anyamata ena achamba akumenya nkulu wina wachimimba chake kamba kakuti nkuluyu anali bwana ndithu nde anthu afodyawo amafuna kumulanda nkuluyu galimoto lake mwa uchifwamba komatu nkuluyu amakaniza ma key-mnyamatayu ataona izi ananva zinphavu zachilendo anathamanga namenya achifwambawo mpaka anathawa

Bwanayo atafusa mnyamatayo dzina lake anayankha iye anauza bwanayo kuti anali DENIS bwanayo atadziwa kut man Denis sanali pa ntchito anapasana ma phon numbers

Tsiku lotsatilalo bwanayo anayimba fon namuuza denis kuti akumane atakumana anatengana nafika pa chinyumba china chokongola atalowa anaona ma offeces ambili mkatimo-bwanayo anaitana anthu onse mkatimo ndipo anafika iye anati”ndapeza mwana okula kula uyu ali apayu wandipulumusa ku imfa dzulo dzuloli-ndipo ameneyu nde akhale wachiwili kwa ine-denis anadabwa koophya ndipo anava ngati azikozele anthu anafika namu haga kunali ma congrats kumeneko

Mwezi utatha anadabwa salary yake itafika kuti inali 2milion iye njenjenje nayo

Patadusa miyezi 6 anaganiza zokaonaso muzi uja anachokera poti anausowa- atafika pa malo ena anapeza anthu akukuntha mayi wina iye anafusa ndipo anthuwo anati anati mayiyo anali nawo ngongole ya 1 million pamozi apa denis analemba cheque cha ndalamayo anthuwo anachoka pa malopo – apa denis anadabwa kuona kuti awa anali mayi ake a msungwana uja ndipo anawathandiza-

ABALE TISAMAONELANE PANSI TONSE NDIFE ANA AMULUNGU-simukuziwa ikugwilani dzanja mawa nde osamanyozana amen

 

 

Advertisements