Umpawi ulipo pamalawi

Lipoti la umoyo ndi chitukuko cha anthu la chaka cha 2016 laika dziko la Malawi pa nambala 170 mwa maiko 188 zomwe zikuthandauza kuti dziko la Malawi lili m’gulu la maiko omwe sakuchita bwino.

Pokhazikitsa lipotili mu mzinda wa Lilongwe Lachitatu mkulu wa bungwe la United Nations kuno ku Malawi Mia Seppo wati dziko la Malawi lili ndi kuthekera kochita bwino koma izi zitenga nthawi.

Akatswiri omvetsa bwino thandauzo la umoyo komanso chitukuko sanabise mawu kuti dziko la Maalwi likadali ndi ntchito yochuluka kuti ikhale ndi anthu omwe ali ndi umoyo wabwino ndi kutukuka.

Mkulu wa bungwe la United Nations kuno ku Malawi Mia Seppo akuvomereza izi: “Kusuntha kuchoka m’gula la maiko ochita bwino kufika pa ochita bwino sikungachitike mwamsanga. Pali zambiri zomwe zikufunika kuchitika, monga kukhala ndi ndondomeko zabwino komanso kugwiritsa ntchito ndalama, zipangizo mopindulira aliyense,”

Dziko la Malawi liri pa nambala 170 mwa maiko 188 pa ntchito zokhudza umoyo ndi chitukuko cha anthu.

Malawi ali m’gulu limodzi ndi maiko monga DRC, Afgjanistan, Ethiopia, Cote D’Iviore ndi Mali omwe sakuchita bwino pa umoyo wa anthu.

Maiko ena omwe anayandikana ndi dziko la Malawi monga Zambia ali m’gulu la pakatikati pochita bwino ndi kusachita bwino pa ntchito za umoyo ndi chitukuko cha anthu. Dziko la Zambia liri pa ndambala 139.

Dziko la Tanzania ngakhale likuchitako bwino lili m’gulu limodzi ndi dziko la Malawi losachita bwino pa ndambala 151 ndipo dziko la Mozambique lili pa nambala 18.

Kaundula wa lipotili amakhudza mbali zosiyanasiyana za umoyo wa munthu, monga mwai was maphunziro, thandizo la za chipatala, ulimi ndi zina zomwe munthu amafuna pa moyo wake wa tsiku ndi tsiku.

Nduna yowona za chuma Goodal Gondwe yati nthawi yakwana yoti anthu m’dziko lino azindikire kuti dziko silingatukuke posiyira ntchito zonse m’manja mwa boma, koma anthu nawo ayenera kulimbikila.

“Anthu amaona ngati chitukuko ndiye kuti munthu akhale ndi ndalama; amange nyumba komanso boma limange nseu koma chitukuko chili m’magawo ambiri. Chachikulu n’chakuti anthu ayenera kulimbikira,” watelo Gondwe.

Lipotili latinso ngakhale maiko akukwaniritsa zina mwa mfundo za chitukuko koma pali anthu ena monga amai, okalamba, anthu othawa kwao kamanso anthu omwe amagonana amuna kapena akazi okhaokha akusalidwa pa ntchito zambiri.

Mu Africa, maiko monga Algeria ndi Tunisia ali m’gulu maiko 100 omwe akuchita bwino pa ntchitozi ndipo maiko monga South Africa, Morocco, Namibia, Ghana, Kenya ndi Zambia ali pakatikati pa maiko omwe akuchita bwino kwamabiri ndi omwe sakuchita bwino.

Advertisements