Dr peter kampalume aku yembekezeka kukhala ndi zokambilana ndi maiko amozambique komaso zimbabwe

 

Nduna ya za umoyo Dr. Peter Kumpalume ikuyembekezeka kukumana ndi nduna za umoyo m’maiko a Mozambique ndi Zimbabwe sabata ino kuti akambirane nkhani zokhudza umoyo m’maiko atatuwa.

Polankhula ndi Zodiak Dr Kumpalume wati imodzi mwa mfundo zomwe akakambirane ndi njira zomwe maikowa angatsate popewa kufala kwa nthenda ya kolera yomwe yapha kale anthu ku Tete m’dziko la Mozambique.

Zipatala za m’dziko muno m’madera a chigwa cha mtsinje wa Shire zathandiza kale anthu odwala nthendayi okwana khumi ndi m’modzi ochokera m’dziko la Mozambique.

“Misonkhano yotere idachitikapo m’mbuyomu koma sipamakhala nduna,” anatero a Kumpalume.

“Nkhani yaikulu pano ndi ya kubuka kwa matenda a kolera ku Tete m’dziko la Mozambique ndipo tikakambirana njira zomwe tingatsate polimbana ndi matendawa kuti maiko onse adzichita zofanana”.

Malingana ndi a Kumpalume, pa msonkhanowo, omwe uchitikire ku Tete, akambirananso nkhani zokhudza umoyo monga njira zomwe maiko atatuwa angatsate popewa kufala kwa nthenda ya chimfine cha mbalame.

Malipoti akusonyeza kuti maiko ena a muno mu Africa monga Uganda akhudzidwa ndi chimfine cha mbalame.

Advertisements