MCp ipambana  pachisankha cha mp wanyumba ya malamulo

20161103125118Chipani chotsutsa cha Kongeresi chaonetsa mbonaona chipani cholamula cha Democratic Progressive mu zisankho za padera zimene zinachitika mu maderaasanu a dziko lino.Chimake cha zisankhozi chinali ku Mchinji kumene amasankha phundu wa nyumba ya malamulo.Kumeneku phungu wakale wa chipani chotsutsa a Billy Kanjira anamwalira zimene zinapangitsa kuti kuchitike chisankho cha padera.

 

 

 

 

 

A chipani cholamula anachita misonkhano yamphamvu ndipo mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika anapita kumeneko kukawaopseza anthu a ku deralo kuti ngati asankhe phungu wa chipani chotsutsa, iwo sazaonanso chitukuko.Koma kuopseza kwa a Mutharika kukuoneka sikunaphule kanthu.Pa zisankho zimene zinachitika lachiwiri, anthuwo anavotelanso phungu wotsutsa wa chipani cha Kongeresi.Kupambana kwa mpando wa phungu kwa chipani cha Kongeresi mu dera la ku Mchinji kunapitilila pamene chipanichi chinapambananso mpando wa Khansala mu deralina ku Kasungu ndi lina ku Dedza.Chipani cholamula cha DPP chinangokwanitsa kupata mipando iwiri basi ya Khansala, wina ku Kasungu ndi wina ku Zomba.

Advertisements