FRANK GABADINHo MHANGO AKUPITILIZA KUONETSA MBWADZA MATIMU ENA

Katswiri ogoletsa zigoli mu timu ya dZiko lino Frank Gabadinho Mhango akupitilira kukhala chipsinjo ku matimu ena ndi kukhala m’dalitso ku timu yake ya Bidvest Wits pomwe usiku wapitawo wathandiza timu yake kupita pa mwamba pa ligi mu usiku omwe za zikulu zachitika mphuzitsi wa timu ya Orando Pirates atatula pansi udindo wake timu yake itagonja 6-1 ndi Supersport.

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

Anali masewero a mbari zonse pa Dobsonville Stadium ku Soweto pakati pa Chippa United komanso Bidvest Wits ndipo mu Mphindi makumi awiri zoyambilira timu ya Chippa ikanatsogola otchinga ku mbuyo wa Wits Thulani Hlatshwayo atalakwitsa koma Katlego Mashego anakanika kagoletsa.Koma mu mphindi 54 anali Gabadinho Mhango yemwe anasumba mpira omwe unatumizidwa ndi Elias Pelembe kugoletsa chigoli chomwe chathandiza Wits kufika pa mwamba pa ligi pomwe Chippa inakali pa nambala 9.Gaba anali ndi mwayi ogoletsa chigoli cha chiwiri koma anakanika kutero kutatsala mphindi khumi ndi zisanu kuti mpira uthe pomwe mpira omwe anamenya Cuthbert Malajila unachotsedwa ndi goloboyi wa Chippa Daniel Akpeyi koma Gaba anakanika kumalizitsa koma pameto pa zonse timu yake yapambana 1-0.full_size_20161102085513

Advertisements